Loading scripture...
Episkopi wa Dayosizi ya Zomba, Ambuye Alfred Mateyu Chaima, alimbikitsa mamembala a bungwe la Legio ya Maria mu mpingo wa Katolika kuti atengere chitsanzo chabwino cha nkhoswe yawo, yomwe ndi Amayi Maria, chopemphelera mpingo ndinso kupilira pamene akumana ndi mavuto mu utumiki wawo.
Ambuye Chaima alankhula izi Lachitatu ku Thondwe Pastoral Centre mu Dayosizi ya Zomba potsekulira msonkhano wapachaka wa tsiku limodzi wa atsogoleri a bungwe la Legio ya Maria omwe wasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a bungwe-li ochokera m’ma Dayosizi onse asanu ndi awiri mu mpingo wa Katolika m’dziko muno.
Ambuye Chaima ati Amayi Maria anali munthu opilira, wachikhulupiliro, omvetsera, odzichepetsa komanso okonda kupemphera, choncho mamembala a bungwe-li akuyenera kutengera chitsanzo chimenechi. Iwo ati izi zithandiza anthu ena kuzindikira ndikumvetsa bwino za Amayi Maria, makamaka udindo wawo mu Mpingo.
Pamenepa, Ambuye Chaima alimbikitsanso atsogoleri-wa kuti zomwe atenga ku nkumano-wu akagawane ndi anzawo ncholinga choti nawonso akhale ozama m’chikhulupiliro.
Polankhulaponso pa msonkhano-wu, mlangizi wa bungwe la Legio ya Maria m’dziko muno, bambo Henry Chimkanda, ati msonkhano ngati uwu umachitika chaka ndi chaka ncholinga chofuna kuwunikirana m’mene atumikilira Mulungu m’magawo osiyana-siyana.
Ndipo president wa bungwe la Legio ya Maria ku dera la Blantyre, Mayi Florence Musasa, ati nkumano-wu uwathandizira kuzamitsa chikhulupiliro chawo mwa Amayi Maria omwe ndi nkhoswe ya bungwe lawo.
Nkumano-wu unachitika pa mutu oti “Kudzamitsa moyo wa Chikhristu modalira Amayi Maria, utumiki wa upostoli wa Legio.”
Comments (0)
Leave a Comment